Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 22:31-40 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

31. Tsono mfumu ya Aramu idalamulira akapitao makumi atatu mphambu ziwiri za magareta ace, niti, Musaponyana ndi anthu ang'ono kapena akuru, koma ndi mfumu ya Israyeli yokha.

32. Ndipo kunali, akapitao a magareta ataona Yehosafati, anati, Zedi uyu ndiye mfumu ya Israyeli imene, napotolokera kukaponyana naye; koma Yehosafati anapfuula.

33. Ndipo pamene akapitao a magareta anaona kuti sindiye mfumu ya Israyeli, anabwerera osampitikitsa.

34. Ndipo munthu anakoka uta wace ciponyeponye, nalasa mfumu ya Israyeli pakati pa maluma a maraya acitsulo; tsono ananena ndi mnyamata wa gareta wace, Tembenuza dzanja lako, nundicotse kunkhondo, popeza ndalasidwa.

35. Ndipo nkhondo inakula tsiku lomwelo, ndipo mfumu inagwirizidwa m'gareta mwace kupenyana ndi Aaramu, natsirizika madzulo; ndipo mwazi unaturuka m'bala pa phaka la gareta.

36. Ndipo mfuu unafikira khamu lonse la nkhondo polowa dzuwa, ndi kuti, Yense kumudzi kwao, ndi yense ku dziko la kwao.

37. Ndipo inafa mfumu, naifikitsa ku Samaria, naika mfumu m'Samaria.

38. Ndipo potsuka garetayo pa thawale la ku Samaria agaru ananyambita mwazi wace, pala pamasamba akazi adama, monga mwa mau a Yehova amene ananenawo.

39. Tsono macitidwe ena a Ahabu, ndi zonse adazicita, ndi nyumba ya minyanga adaimanga, ndi midzi yonse adaimanga, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?

40. Ndipo Ahabu anagona ndi makolo ace; ndi Ahaziya mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 22