Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 22:22-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Nati, Ndidzaturuka, ndidzakhala mzimu wonama m'kamwa mwa aneneri ace onse. Nati, Udzamnyengadi, nudzakhozanso; turuka, ukatero kumene.

23. Ndipo tsopano taonani, Yehova waika mzimu wonama m'kamwa mwa aneneri anu onse awa, ndipo Yehova ananena coipa ca inu.

24. Pamenepo Zedekiya mwana wa Kenana anasendera, napanda Mikaya patsaya, nati, Mzimu wa Yehova wandicokera bwanji, kulankhula ndi iwe?

25. Mikaya nati, Taona, udzapenya tsiku lolowa iwe m'cipinda ca pakati kubisala.

26. Pamenepo inati mfumu ya Israyeli, Tengani Mikaya, mumbweze kwa Amoni kalonga wa mudzi, ndi kwa Yoasi mwana wa mfumu;

27. ndipo muziti, Itero mfumu, Khazikani uyu m'kaidi, mumdyetse cakudya ca nsautso, ndi madzi a nsautso, mpaka ndikabwera ndi mtendere.

28. Ndipo Mikaya anati, Mukabwera ndithu ndi mtendere Yehova sanalankhula mwa ine. Nati, Mvetsani, anthu inu nonse.

29. Tsono mfumu ya Israyeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakwera ku Ramoti Gileadi.

30. Ndipo mfumu ya Israyeli inanena ndi Yehosafati, Ine ndidzadzizimbaitsa, ndi kulawa kunkhondo, koma bvala iwe zobvala zako zacifumu. Ndipo mfumu ya Israyeli inadzizimbaitsa, nilowa kunkhondo.

31. Tsono mfumu ya Aramu idalamulira akapitao makumi atatu mphambu ziwiri za magareta ace, niti, Musaponyana ndi anthu ang'ono kapena akuru, koma ndi mfumu ya Israyeli yokha.

32. Ndipo kunali, akapitao a magareta ataona Yehosafati, anati, Zedi uyu ndiye mfumu ya Israyeli imene, napotolokera kukaponyana naye; koma Yehosafati anapfuula.

33. Ndipo pamene akapitao a magareta anaona kuti sindiye mfumu ya Israyeli, anabwerera osampitikitsa.

34. Ndipo munthu anakoka uta wace ciponyeponye, nalasa mfumu ya Israyeli pakati pa maluma a maraya acitsulo; tsono ananena ndi mnyamata wa gareta wace, Tembenuza dzanja lako, nundicotse kunkhondo, popeza ndalasidwa.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 22