Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 20:35-43 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

35. Ndipo wina wa ana a aneneri ananena ndi mnzace mwa mau a Yehova, Undikanthe ine, Koma munthuyo anakana kumkantha.

36. Ndipo ananena naye, Popeza sunamvera mau a Yehova, taona, utalekana nane mkango udzakupha, Ndipo m'mene atalekana naye, mkango unampeza, numupha.

37. Ndipo amene uja anakomana ndi munthu wina, nati, Undikanthe. Namkantha munthuyu, namtema pomkantha.

38. Pamenepo mneneriyo anamuka, nadikira mfumu pamseu, nadzizimbaitsa ndi mpango pamaso pace.

39. Ndipo popitapa mfumu, anapfuula kwa mfumu, nati, Kapolo wanu analowa pakati pa nkhondo, ndipo taonani, munthu anapambuka nabwera ndi munthu kwa ine, nati, Tasunga munthu uyu; akasowa ndi cifukwa ciri conse moyo wako udzakhala m'malo mwa moyo wace, kapena udzalipa talenti la siliva.

40. Tsono pocita kapolo wanu apo ndi apo ndapeza palibe. Ndipo mfumu ya Israyeli inati kwa iye, Mlandu wako ukutsutsa momwemo, wadziweruza wekha.

41. Ndipo iye anafulumira kucotsa mpango kumaso kwace, ndi mfumu ya Israyeli inaona kuti anali mmodzi wa aneneri.

42. Niti kwa iye, Atero Yehova, Popeza wataya m'dzanja lako munthu uja ndinati ndimuononge konse, moyo wako udzakhala m'malo mwamoyo wace, ndi anthu ako m'malo mwa anthu ace.

43. Pamenepo mfumu ya Israyeli inamka kwao wamsunamo ndi wokwiya, nafika ku Samaria.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 20