Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 2:42-46 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

42. Ndipo mfumu inatuma munthu kukaitana Simeyi, niti kwa iye, Kodi sindinakulumbiritsa pa Yehova ndi kukucenjeza, kuti, Tadziwa ndithu, kuti tsiku lakuturuka iwe ndi kukayenda kwina konse udzafa ndithu? Ndipo iwe unati kwa ine, Mau amene ndawamva ndi abwino.

43. Sunasunga cifukwa ninji lumbiro la pa Yehova, ndi lamulo lija ndinakulamulira iwe?

44. Tsono mfumu inanenanso ndi Simeyi, Udziwa iwe coipa conse mtima wako umadziwaco, cimene udacitira Davide atate wanga; cifukwa cace Yehova adzakubwezera coipa cako pamutu pako mwini.

45. Koma mfumu Solomo adzadalitsika, ndi mpando wacifumu wa Davide udzakhazikika pamaso pa Yehova ku nthawi yamuyaya.

46. Pamenepo mfumu inalamulira Benaya mwana wa Yehoyada, ndipo iye anaturuka namkwera, namwalira iye. Ndipo ufumu unakhazikika m'dzanja la Solomo.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 2