Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 19:19-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Tsono anacokako, napeza Elisa mwana wa Safati alikukoketsa cikhasu ng'ombe ziwiri ziwiri magori khumi ndi awiri, iye yekha anakhala pa gori lakhumi ndi ciwiri; ndipo Eliya anamka kunali iyeyo, naponya copfunda cace pa iye.

20. Ndipo iye anasiya ng'ombe zija, namthamangira Eliya, nati, Ndiloleni ndithange ndakapsompsona atate wanga ndi amai wanga; nditatero ndidzakutsatani. Nati iye, Bwerera, ndakucitanji?

21. Ndipo anabwerera panali iye uja, natengako ng'ombe ziwiri, nazipha, naphikira nyama yace ndi zipangizo za zocitira nazo ng'ombe, napatsa anthu adye. Atatero, ananyamuka, natsata Eliya, namtumikira.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 19