Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 18:36-46 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

36. Ndipo kunali, nthawi ya kupereka nsembe yamadzulo, Eliya mneneri anasendera, nati, Yehova Mulungu wa Abrahamu ndi Isake ndi Israyeli, lero kudziwike kuti Inu ndinu Mulungu wa Israyeli, ndi ine mtumiki wanu, kuti mwa mau anu ndacita zonsezi.

37. Ndimvereni Yehova, ndimvereni, kuti anthu awa adziwe kuti Inu Yehova ndinu Mulungu, ndi kuti Inu mwabwezanso mitima yao.

38. Pamenepo moto wa Yehova unagwa, nutentha nsembe yopsereza, ndi nkhuni, ndi miyala, ndi pfumbi, numwereretsa madzi anali mumcera.

39. Ndipo anthu onse anaona, nagwa nkhope zao pansi, nati, Yehova ndiye Mulungu, Yehova ndiye Mulungu.

40. Ndipo Eliya anati kwa iwo, Gwirani aneneri a Baala, asapulumuke ndi mmodzi yense. Nawagwira, ndipo Eliya ana pita nao ku mtsinje wa Kisoni, nawapha pamenepo.

41. Ndipo Eliya ananena ndi Ahabu, Nyamukani, idyani, imwani; popeza kumveka mkokomo: wa mvula yambiri.

42. Ndipo Ahabu anakadya, namwa; koma Eliya anakwera pamwamba pa Karimeli, nagwadira pansi, naika nkhope yace pakati pa maondo ace.

43. Ndipo anati kwa mnyamata wace, Kwera kapenyerere kunyanja. Iye nakwera, napenyetsetsa, nati, Kulibe kanthu. Nati, Bwerezanso kasanu ndi kawiri.

44. Ndipo kunali kacisanu ndi ciwiri anati, Taonani, kwaturuka kunyanja kamtambo konga dzanja la munthu. Nati iye, Kauze Ahabu, kuti, Mangani gareta, tsikani, mvula Ingakutsekerezeni.

45. Ndipo kunali, polinda kanthawi, thambo linada ndi mitambo ndi mphepo, nigwa mvula yaikuru. Ndipo Ahabu anayenda m'gareta, namuka ku Yezreeli.

46. Ndipo dzanja la Yehova tinakhala pa Eliya; namanga iye za m'cuuno mwace, nathamanga m'tsogolo mwa Ahabu ku cipata ca Yezreeli.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 18