Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 16:8-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo caka ca makumi awiri mphambu zisanu ndi cimodzi ca Asa mfumu ya Yuda, Ela mwana wa Basa analowa ufumu wa Israyeli ku Tiriza, nakhala mfumu zaka ziwiri.

9. Ndipo mnyamata wace Zimri, ndiye woyang'anira dera lina la magareta ace, anampangira ciwembu; koma iye anali m'Tiriza kumwa ndi kuledzera m'nyumba ya Ariza, ndiye woyang'anira nyumba m'Tiriza.

10. Nalowamo Zimri, namkantha, namupha caka ca makomi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri ca Asa mfumu ya Yuda, nalowa ufumu m'malo mwace.

11. Ndipo kunali, atalowa ufumu wace, nakhala pa mpando wacifumu wace, anawakantha onse a m'nyumba ya Basa, osamsiyira mwana wamwamuna ndi mmodzi yense, kapena wa abale ace, kapena wa mabwenzi ace.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 16