Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 16:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo mau a Yehova akutsutsa Basa anadza kwa Yehu mwana wa Hanani, nati,

2. Popeza ndinakukuza iwe kucokera kupfumbi, ndi kukuika iwe mfumu ya anthu anga Israyeli, koma iwe unayenda m'njira ya Yerobiamu, ndi kucimwitsa anthu anga Israyeli, kuputa mkwiyo wanga ndi macimo ao;

3. taona, ndidzacotsa psiti Basa ndi nyumba yace, ndipo ndidzafanizitsa nyumba yako ndi nyumba ya Yerobiamu mwana wa Nebati,

4. Agaru adzadya ali yense wa Basa amene adzafera m'mudzi, ndipo amene adzafera m'thengo zidzamudya mbalame za m'mlengalenga.

5. Tsono macitidwe ena a Basa, ndi nchito zace, ndi mphamvu zace, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?

6. Nagona Basa ndi makolo ace, naikidwa ku Tiriza; ndipo Ela mwana wace analowa ufumu m'malo mwace.

7. Ndiponso mau a Yehova anadza ndi dzanja la mneneri Yehu mwana wa Hanani, kutsutsa Basa ndi nyumba yace, cifukwa ca zoipa zonse anazicita iye pamaso pa Yehova; popeza anaputa mkwiyo wace ndi macitidwe a manja ace, nafanana ndi nyumba ya Yerobiamu; ndiponso popeza anaikantha.

8. Ndipo caka ca makumi awiri mphambu zisanu ndi cimodzi ca Asa mfumu ya Yuda, Ela mwana wa Basa analowa ufumu wa Israyeli ku Tiriza, nakhala mfumu zaka ziwiri.

9. Ndipo mnyamata wace Zimri, ndiye woyang'anira dera lina la magareta ace, anampangira ciwembu; koma iye anali m'Tiriza kumwa ndi kuledzera m'nyumba ya Ariza, ndiye woyang'anira nyumba m'Tiriza.

10. Nalowamo Zimri, namkantha, namupha caka ca makomi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri ca Asa mfumu ya Yuda, nalowa ufumu m'malo mwace.

11. Ndipo kunali, atalowa ufumu wace, nakhala pa mpando wacifumu wace, anawakantha onse a m'nyumba ya Basa, osamsiyira mwana wamwamuna ndi mmodzi yense, kapena wa abale ace, kapena wa mabwenzi ace.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 16