Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 14:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Nthawi yomweyo Abiya mwana wa Yerobiamu anadwala.

2. Ndipo Yerobiamu ananena ndi mkazi wace, Unyamuke, nudzizimbaitse, ungadziwike kuti ndiwe mkazi wa Yerobiamu, nupite ku Silo; taona, kumeneko kuli Ahiya mneneri uja anandiuza ine ndidzakhala mfumu ya anthu awa.

3. Nupite nayo mikate khumi, ndi timitanda, ndi cigulu ca uci, numuke kwa iye; adzakuuza m'mene umo akhalire mwanayo.

4. Natero mkazi wa Yerobiamu, nanyamuka namka ku Silo, nalowa m'nyumba ya Ahiya. Koma Ahiya sanatha kupenya, popeza maso ace anali tong'o, cifukwa ca ukalamba wace.

5. Ndipo Yehova ananena ndi Ahiya, Taona, mkazi wa Yerobiamu akudza kukufunsa za mwana wace, popeza adwala; udzanena naye mwakuti mwakuti; popeza kudzakhala pakulowa iye adzadzizimbaitsa.

6. Ndipo kunacitika, pamene Ahiya anamva mgugu wa mapazi ace alinkulowa pakhomo, anati, Lowa mkazi iwe wa Yerobiamu, wadzizimbaitsiranji? pakuti ine ndatumidwa kwa iwe ndi mau olasa.

7. Kauze Yerobiamu, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Ndingakhale ndinakukulitsa pakati pa anthu, ndi kukukhalitsa mfumu ya anthu anga Aisrayeli,

8. ndipo ndinalanda nyumba ya Davide ufumu, ndi kuupereka kwa iwe, koma sunafanana ndi Davide mtumiki wanga uja, amene anasunga malamulo anga, nanditsata ndi mtima wace wonse kucita zolunjika zokha zokha pamaso panga;

9. koma wacimwa koposa onse akale, nukadzipangira milungu yina ndi mafano yoyenga kundikwiyitsa, nunditaya Ine kumbuyo kwako;

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 14