Natero mkazi wa Yerobiamu, nanyamuka namka ku Silo, nalowa m'nyumba ya Ahiya. Koma Ahiya sanatha kupenya, popeza maso ace anali tong'o, cifukwa ca ukalamba wace.