Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 12:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Rehabiamu anamka ku Sekemu, popeza Aisrayeli onse anadza ku Sekemu kumlonga ufumu.

2. Ndipo kunali kuti Yerobiamu mwana wa Nebati anacimva akali m'Aigupto, kumene anathawira kucokera ku maso a Solomo mfumu, pakuti Yerobiamu anakhala ku Aigupto.

3. Ndipo anatuma akukamuitana. Ndipo Yerobiamu ndi msonkhano wonse wa Israyeli anadza, nalankhulana ndi Rehabiamu, nati,

4. Atate wa nu analemeretsa gori lathu, ndipo inu tsono pepuzaniko nchito zosautsa za atate wanu, ndi gori lolemera lace limene anatisenza, ndipo tidzakutumikirani.

5. Ndipo iye anati kwa iwo, Bamukani, mukagone masiku atatu, pamenepo mukabwera kwa ine. Ndipo anthu anamuka.

6. Ndipo mfumu Rehabiamu anafunsira kwa mandoda, amene anaimirira pamaso pa Solomo atate wace, akali moyoiyeyo, nati, Inu mundipangire bwanji kuti ndiyankhe anthu awa?

7. Ndipo iwo anamuuza kuti, Mukakhala inu mtumiki wa anthu awa lero, ndi kuwatumikira ndi kuwayankha ndi kukamba nao mau okoma, tsono iwo adzakhala cikhalire atumiki anu.

8. Koma iye analeka uphungu wa mandodawo, umene anampangirawo, nakafunsira kwa acinyamata anzace oimirira pamaso pace,

9. nati kwa lwo, Kodi inu mundipangire bwanji kuti tiyankhe anthu awa anandiuza ine, kuti, Mupepuze gori limene atate wanu anatisenza ife?

10. Ndipo acinyamata anzace ananena naye, Dati, Mzitero ndi anthu awa adalankhula nanu, nati, Atate wanu analemeretsa gori lathu, koma inu mutipepuzire limenelo; mzitero nao, Kanense wanga adzaposa m'cuuno mwa atate wanga.

11. Ndipo tsopano, popeza atate wanga anakusenzani gori lolemera, ine ndidzaonjezerapo pa gori lanu, atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.

12. Ndipo Yerobiamu ndi anthu onse anabwera kwa Rehabiamu tsiku lacitatu monga momwe anawauzira mfumu, nati, Bweraninso kwa ine tsiku lacitatu.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 12