Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 1:39-44 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

39. Ndipo Zadoki wansembe anatenga nyanga ya mafuta inali m'Cihema, namdzoza Solomo. Ndipo iwo anaomba lipenga, ndi anthu onse anati, Mfumu Solomo akhale ndi moyo.

40. Ndipo anthu onse anakwera namtsata, naliza zitoliro, nakondwera ndi kukondwera kwakukuru, kotero kuti pansi panang'ambikandiphokosolao.

41. Ndipo Adoniya ndi oitanidwa onse anali ndi iye analimva atatha kudya. Ndipo Yoabu, pakumva kuomba kwa lipengalo, anati, Phokosolo ndi ciani kuti m'mudzi muli cibumo?

42. iye akali cilankhulire, taona, walowa Yonatani mwana wa Abyatara wansembe, ndipo Adoniya anati, Lowa, popeza ndiwe munthu wamphamvu, nubwera nao uthenga wabwino.

43. Ndipo Yonatani anayankha, nati kwa Adoniya, Zedi Davide mbuye wathu mfumu walonga Solomo ufumu:

44. ndipo mfumu yatumanso Zadoki wansembe, ndi Natani mneneri, ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndi Akereti, ndi Apeleti aja, namkweza iye pa nyuru ya mfumu.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 1