Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 1:30-36 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

30. zedi monga umo ndinalumbirira iwe pa Yehova Mulungu wa Israyeli, ndi kuti, Zoonadi Solomo mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wacifumu m'malo mwa ine, zedi nditero lero lomwe.

31. Pamenepo Batiseba anaweramitsa pansi nkhope yace, nalambira mfumu, nati, Mbuye wanga mfumuakhale ndi moyo nthawi zamuyaya.

32. Ndipo mfumu Davide anati, Kandiitanireni Zadoki wansembeyo, ndi Natani mneneriyo, ndi Benaya mwana wa Yehoyada. Iwo nalowa pamaso pa mfumu.

33. Ndipo mfumu inati kwa iwo, Tengani akapolo a mfumu yanu, nimukweze Solomo mwana wanga pa nyuru yanga yanga, nimutsikire naye ku Gihoni.

34. Ndipo Zadoki wansembe ndi Natani mneneri akamdzoze kumeneko akhale mfumu ya Israyeli; ndipo muombe lipenga, ndi kuti, Mfumu Solomo akhale ndi moyo.

35. Pamenepo mumtsate iye, iye nadzadza nadzakhala pa mpando wanga wacifumu, popeza adzakhala iyeyu mfumu m'malo mwanga; ndipo ndamuika iye akhale mtsogoleri wa lsrayeli ndi Yuda.

36. Ndipo Benaya mwana wa Yehoyada anayankha mfumu, nati, Amen, ateronso Yehova Mulungu wa mbuye wanga mfumu.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 1