Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 1:1-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. NDIPO mfumu Davide anakalamba nacuruka masiku ace; ndipo iwo anampfunda ndi zopfunda, koma iye sanafundidwa.

2. Pamenepo anyamata ace ananena naye, Amfunire mbuye wanga mfumu namwali, aimirire pamaso pa mfumu namsunge; nagone m'mfukato mwanu, kuti mbuye mfumu yanga afundidwe.

3. Tsono anafunafuna m'malire monse a Israyeli namwali wokongola, napeza Abisagi wa ku-Sunamu, nabwera naye kwa mfumu.

4. Ndipo namwaliyo anali wokongola ndithu, namasunga mfumu namtumikira; koma mfumu sinamdziwa.

5. Pamenepo Adoniya mwana wa Hagiti anadzikuza, nati, Ndikhala mfumu ndine; nadzikonzera agareta ndi apakavalo ndi anthu makumi asanu omtsogolera mothamanga.

6. Ndipo atate wace sadambvuta masiku ace onse, ndi kuti, Wlitero cifukwa ninji? Ndiponso anali munthu wokongola ndithu; napondana ndi Abisalomu.

7. Ndipo anapangana ndi Yoabu mwana wa Zeruya, ndi Abyatara wansembeyo; ndipo amenewo anamtsata Adoniya namthandiza.

8. Koma Zadoki wansembe, ndi Benaya mwana wace wa Yehoyada, ndi Natani mneneri, ndi Simeyi, ndi Reyi, ndi anthu amphamvu aja adali ndi Davide, sanali ndi Adoniya.

9. Ndipo Adoniya anapha nkhosa ndi ng'ombe ndi nyama zonona pamwala pa Zoheleti, uli pafupi ndi citsime ca Rogeli, naitana abale ace onse ana a mfumu, ndi anthu onse a Yuda anayamata a mfumu;

10. koma Natani mneneriyo, ndi Benaya, ndi anthu amphamvu aja, ndi Solomo mbale wace, sanawaitana.

11. Pamenepo Natani ananena ndi Batiseba amace wa Solomo, nati, Kodi sunamva kuti Adoniya mwana wa Hagiti walowa ufumu, ndipo Davide mbuye wathu sadziwa?

12. Ubwere tsono, ndikupangire, kuti usunge moyo wako, ndi moyo wa mwana wako Solomo.

13. Muka nulowe kwa mfumu Davide, nukati kwa iye, Mbuye wanga mfumu, kodi simunalumbirira mdzakazi wanu, ndi kuti, Zedi Solomo mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wadfumu? ndipo Adoniya akhaliranji mfumu?

14. Taona, uli cilankhulire ndi mfumu, inenso ndidzalowa pambuyo pako, ndi kutsimikiza mau ako.

15. Pamenepo Batiseba analowa kwa mfumu kucipinda; ndipo mfumuyo inali yokalamba ndithu; ndipo Abisagi wa ku Sunamu anali kutumikira mfumu.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 1