16. ndi Yuda mwana wa Yakobo, ndi Yudase Isikariote, amene anali wompereka iye.
17. Ndipo iye anatsika nao, naima pacidikha, ndi khamu lalikuru la ophunzira ace, nw unyinji waukuru wa anthu a ku Yudeya lonse ndi Yerusalemu, ndi a ku mbali ya nyanja ya ku Turo ndi Sidoni, amene anadza kudzamva iye ndi kudzaciritsidwa nthenda zao;
18. ndipo obvutidwa ndi mizimu yonyansa anaciritsidwa,
19. ndi khamu lonse lija linafuna kumkhudza iye; cifukwa munaturuka mphamvu mwa iye, niciritsa onsewa.
20. Ndipo iye anakweza maso ace kwa ophunzira ace, nanena, Odala osauka inu; cifukwa uli wanu ufumu wa Mulungu.
21. Odala inu akumva njala tsopano; cifukwa mudzakhuta. Odala inu akulira tsopano; cifukwa mudzaseka.
22. Odala inu, pamene anthu adzada inu, nadzapatula inu, nadzatonza inu, nadzalitaya dzina lanu monga loipa, cifukwa ca Mwana wa munthu.
23. Kondwerani tsiku lomweli, tumphani ndi cimwemwe; pakuti onani, mphotho zanu nzazikuru Kumwamba; pakuti makolo ao anawacitira aneneri zonga zomwezo.
24. Koma tsoka inu eni cuma! cifukwa mwalandira cisangalatso canu.