14. Ndipo linga la mudzi linakhala nao maziko khumi ndi awiri, ndi pomwepo maina khumi ndi awiri a atumwi khumi ndi awiri a Mwanawankhosa.
15. Ndipo iye wakulankhula ridi ine anali nao muyeso, bango lagolidi, kuti akayese mzindawo, ndi zipata zace, ndi linga lace.
16. Ndipo mzinda ukhala wampwamphwa; utali wace ulingana ndi kupingasa kwace: ndipo anayesa mzinda ndi bangolo, mastadiya zikwi khumi ndi ziwiri; utali wace, ndi kupingasa kwace, ndi kutalika kwace zilingana.
17. Ndipo anayesa linga lace, mikono zana mphambu makumi anai kudza zinai, muyeso wa munthu, ndiye mngelo.