Ndipo ndinaona ngati nyanja yamandala yosanganiza ndi moto; ndipo iwo amene anaeilaka ciromboco, ndi fano lace ndi ciwerengero ca dzina lace, anaimirira pa nyanja ya mandala, nakhala nao azeze a Mulungu.