1. Ndipo ndinaimirira pa mcenga wa nyanja.Ndipo ndinaona cirombo cirinkuturuka m'nyanja, cakukhala nazo nyanga khumi, ndi mitu isanu ow iwiri, ndi pa nyanga zace nduwira zacifumu khumi, ndi pamitu pace maina a mwano.
2. Ndipo cirombo ndinacionaco cinafanana ndi nyalugwe, ndi mapazi ace ngati mapazi a fisi, ndi pakamwa pace ngati pakamwa pa mkango; ndipo cinjoka cinampatsa iye mphamvu yace, ndi mpando wacifumu wace, ndi ulamuliro waukuru.
3. Ndipo umodzi wa mitu yace unakhala ngati unalasidwa kufikira imfa; ndipo bala lace la kuimfa lidapola; ndipo dziko lonse linazizwa potsata ciromboco;
4. ndipo analambira cinjoka, cifukwa cinacipatsa ulamuliro ciromboco; ndipo analambira cirombo ndi kunena, Manana ndi cirombo ndani? Ndipo akhoza ndani kugwira nkhondo naco?
5. Ndipo anacipatsa ico m'kamwa molankhula zazikuru ndi zamwano; ndipo anacipatsa ulamuliro wa kutero miyezi makumi anai ndi iwiri.