7. komatu m'masiku a mau a mngelo wacisanu ndi ciwiri m'mene iye adzayamba kuomba, pamenepo padzatsirizika cinsinsi ca Mulungu, monga analalikira kwa akapolo ace aneneri.
8. Ndipo mau ndinawamva ocokera Kumwamba, analankhulanso nane, nanena, Muka, tenga buku lofunyululalom'dzanja la mngelo wakuimirira panyanja ndi padziko.
9. Ndipo ndinamuka kwa mngelo, ndi kunena naye, Ndipatse kabukuko. Ndipo ananena ndi ine, Dzatenge, nudye; ndipo kadzawawitsa m'mimbamwako, komatu m'kamwa mwako kadzazuna ngati uci.