12. Ndi malire a kumadzulo anali ku Nyanja Yaikuru ndiwo malire ace. Awa ndi malire a ana a Yuda pozungulira monga mwa mabanja ao.
13. Koma Yoswa anampatsa Kalebe mwana wa Yefune gawo mwa ana a Yuda, monga Yehova adamlamulira, ndiwo mudzi wa Ariba, ndiye atate wa Anaki, ndiwo Hebroni.
14. Ndipo Kalebe anaingitsako ana amuna atatu a Anaki, ndiwo Sesai, ndi Ahimani, ndi Talimai, ana a Anaki.
15. Nakwera komweko kumka kwa nzika za Dibiri; koma kale dzina la Dibiri ndilo Kiriyati-Seferi.
16. Ndipo Kalebe anati, iye amene akantha Kiriyati-Seferi, naulanda, yemweyo ndidzampatsa Akisa mwana wanga akhale mkazi wace.
17. Ndipo Otiniyeli mwana wa Kenazi, mbale wace wa Kalebe, anaulanda; ndipo anampatsa Akisa mwana wace akhale mkazi wace.
18. Ndipo kunali, m'mene anamdzera, anamkangamiza mwamuna wace kuti apemphe atate wace ampatse munda; ndipo anatsika pa buru; pamenepo Kalebe ananena naye, Ufunanji?
19. Nati iye, Mundipatse dalitso; popeza mwandipatsa dziko la kumwela, ndipatseninso zitsime za madzi. Pamenepo anampatsa zitsime za kumtunda, ndi zitsime za kunsi.
20. Ici ndi colowa ca pfuko la ana a Yuda monga mwa mabanja ao.
21. Ndipo midzi ya ku malekezero a pfuko la ana a Yuda ku malire a Edomu, kumwela ndiwo, Kabizeeli ndi Ederi, ndi Yaguri;