5. Ndipo Yehova ananena kwa ine kaciwirinso, nati,
6. Popeza anthu awa akana madzi a Silowa, amene ayenda pang'ono pang'ono, nakondwerera mwa Rezini ndi mwa mwana wa Remaliya;
7. cifukwa cace, taonani, Ambuye atengera pa iwo madzi a Nyanja, olimba ndi ambiri, kunena mfumu ya Asuri ndi ulemerero wace wonse; ndipo iye adzadzala mphaluka zace zonse, nadzasefukira pamtunda ponse.
8. Ndipo iye adzapitapitakulowa m'Yuda; adzasefukira, napitirira; adzafikira m'khosi; ndi kutambasula kwa mapiko ace, kudzakwanira dziko lanu m'citando mwace, inu Imanueli.
9. Citani phokoso, anthu inu, koma mudzatyokatyoka; cherani khutu, inu nonse a maiko akutari; kwindani nokha, koma mudzatyokatyoka; kwindani nokha, koma mudzatyokatyoka.