1. Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwakutsegulidwa kwa m'ndende;
2. ndikalalikire caka cokomera Yehova, ndi tsiku lakubwezera la Mulungu wathu; ndikatonthoze mtima wa onse amene akulira maliro;
3. ndikakonzere iwo amene alira maliro m'Ziyoni, ndi kuwapatsa cobvala kokometsa m'malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m'malo mwa maliro, cobvala ca matamando m'malo mwa mzimu wopsinjika; kuti iwo achedwe mitengo ya cilungamo yakuioka Yehova, kuti Iye alemekezedwe.
4. Ndipo iwo adzamanga mabwinja akale, nadzamanga pa miunda yakale, nadzakonzanso midzi yopasuka, mabwinja a mibadwo yambiri.
5. Ndipo alendo adzaimirira ndi kudyetsa magulu ako, ndi anthu akunja adzakhala olima ako, ndi kukukonzera minda yamphesa.
6. Koma inu mudzachedwa ansembe a Yehova; anthu adzakuyesani inu atumiki a Mulungu wathu; inu mudzadya cuma ca amitundu, nimudzalowa mu ulemerero wao.
7. M'malo mwa manyazi anu, owirikiza; ndi citonzo iwo adzakondwera ndi gawo lao; cifukwa cace iwo adzakhala naco m'dziko mwao colowa cowirikiza, adzakhala naco cikondwerero cosatha.
8. Pakuti Ine Yehova ndikonda ciweruziro, ndida cifwamba ndi coipa; ndipo ndidzawapatsa mphotho yao m'zoonadi; ndipo ndidzapangana nao pangano losatha.