Ndipo iwo amene adzakhala a iwe adzamanga malo akale abwinja; udzautsa maziko a mibadwo yambiri; udzachedwa Wokonza pogumuka, Wakubwezera njira zakukhalamo.