5. Usaope; pakuti Ine ndiri ndi iwe; ndidzatenga mbeu zako kucokera kum'mawa, ndi kusonkhanitsa iwe kucokera kumadzulo.
6. Ine ndidzati ndi kumpoto, Pereka; ndi kumwera, Usaletse; bwera nao ana anga amuna kucokera kutari, ndi ana anga akazi kucokera ku malekezero a dziko lapansi;
7. yense wochedwa dzina langa, amene ndinamlenga cifukwa ca ulemerero wanga; ndinamuumba iye; inde, ndinampanga iye.
8. Turutsani anthu akhungu, amene ali ndi maso, ndi agonthi, amene ali ndi makutu.
9. Amitundu onse asonkhane pamodzi, ndi anthu aunjikane; ndani mwa iwo anganene ici ndi kuonetsa ife zinthu zakale? atenge mboni zao, kuti abvomerezeke ndi olungama; pena amve, nanene zoonadi.