5. Yehova wakwezedwa; pakuti akhala kumwamba; Iye wadzaza Ziyoni ndi ciweruzo ndi cilungamo.
6. Ndipo kudzakhala cilimbiko m'nthawi zako, cipulumutso cambiri, nzeru ndi kudziwa; kuopa kwa Yehova ndiko cumacace.
7. Taonani, olimba mtima ao angopfuula kunja, mithenga ya mtendere ilira kowawa.
8. Njira zamakwalala zikufa, kulibe woyendamo; Asuri watyola cipangano, wanyoza midzi, sasamalira anthu.
9. Dziko lilira maliro ndi kulefuka; Lebano ali ndi manyazi, nafota; Saroni afanana ndi cipululu; pa Basana ndi Karimeli papukutika.
10. Tsopano ndidzauka, ati Yehova; tsopano ndidzanyamuka, tsopano ndidzakwezedwa.
11. Inu mudzatenga pakati ndi mungu, mudzabala ziputu; mpweya wanu ndi moto umene udzakumarizani inu.
12. Ndipo mitundu ya anthu idzanga potentha miyala yanjeresa; monga minga yodulidwa, nitenthedwa ndi moto.
13. Imvani inu amene muli kutari, cimene ndacita ndi inuamene muli pafupi, bvomerezani mphamvu zanga,
14. Ocimwa a m'Ziyoni ali ndi mantha, kunthunthumira kwadzidzimutsa anthu opanda Mulungu. Ndani mwa ife adzakhala ndi moto Wakunyeketsa? ndani mwa ife adzakhala ndi zotentha zacikhalire?
15. Iye amene ayenda molungama, nanena molunjika; iye amene anyoza phindu lonyenga, nasansa manja ace kusalandira zokometsera milandu, amene atseka makutu ace kusamva za mwazi, natsinzina maso ace kusayang'ana coipa;
16. iye adzakhala pamsanje; malo ace ocinjikiza adzakhala malinga amiyala; cakudya cace cidzapatsidwa kwa iye; madzi ace adzakhala cikhalire.
17. Maso ako adzaona mfumu m'kukongola kwace; iwo adzaona dziko lakutari.
18. Mtima wako udzaganizira zoopsya; mlembi ali kuti? ali kuti iye amene anayesa msonkho? ali kuti iye amene anawerenga nsanja?
19. Iwe sudzaona anthu aukali, anthu a mau anthulu, amene iwe sungazindikire; a lilume lacibwibwi, limene iwe sungalimve.
20. Tayang'ana pa Ziyoni, mudzi wa mapwando athu; maso ako adzaona Yerusalemu malo a phe, cihema cimene sicidzasunthidwa, ziciri zace sizidzazulidwa konse, zingwe zace sizidzadulidwa.