4. Ndiponso udzati kwa iwo, Atero Yehova, Kodi adzagwa, osaukanso? Kodi wina adzacoka, osabweranso?
5. Bwanji abwerera anthu awa a Yerusalemu cibwererere? agwiritsa cinyengo, akana kubwera.
6. Ndinachera khutu, ndinamva koma sananena bwino; panalibe munthu amene anatembenuka kusiya zoipa zace, ndi kuti, Ndacita ciani? yense anatembenukira njira yace, monga akavalo athamangira m'nkhondo.
7. Inde, cumba ca mlengalenga cidziwa nyengo zace; ndipo njiwa ndi namzeze ndi cingaru ziyang'anira nyengo yakufika kwao; koma anthu anga sadziwa ciweruziro ca Yehova.
8. Bwanji muti, Tiri ndi nzeru ife, ndi malamulo a Yehova ali ndi ife? Koma, taona, peni lonyenga la alembi lacita zonyenga,
9. Anzeru ali ndi manyazi, athedwa nzeru nagwidwa; taonani, akana mau a Yehova; ali nayo nzeru yotani?
10. Cifukwa cace ndidzapereka akazi ao kwa ena, ndi minda yao kwa iwo adzalowamo; pakuti onse kuyambira wamng'ono kufikira wamkuru asirirasirira; kuyambira mneneri kufikira wansembe onse acita zonyenga.