Cifukwa cace mkango woturuka m'nkhalango udzawapha, ndi mmbulu wa madzulo udzawafunkha, nyalugwe adzakhalira m'midzi mwao, onse amene aturukamo adzamwetulidwa; pakuti zolakwa ziri zambiri, ndi mabwerero ao acuruka.