Cifukwa cace Yehova atero za Yehoyakimu mfumu ya Yuda: Adzasowa wokhala pa mpando wacifumu wa Davide; ndipo mtembo wace udzaponyedwa usana kunja kuli dzuwa, ndi usiku kuli cisanu.