17. Pakuti Yehova atero: Davide sadzasowa munthu wokhala pa mpando wacifumu wa nyumba ya Israyeli;
18. ndiponso ansembe sadzasowa munthu pamaso panga wakupereka nsembe zopsereza, ndi kutentha nsembe zaufa, ndi wakucita nsembe masiku onse.
19. Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya, kuti,
20. Ngati mukhoza kuswa pangano langa la usana ndi pangano langa la usiku, kuti usakhalenso usana ndi usiku m'nyengo yao;
21. pamenepo pangano langa lidzasweka ndi Davide mtumiki wanga, kuti asakhale ndi mwana wamwamuna wakulamulira pa mpando wa ufumu wace; ndiponso ndi Alevi ansembe, atumiki anga.
22. Monga khamu la kuthambo silingathe kuwerengedwa, ndi mcenga wa kunyanja sungathe kuyesedwa; comweco ndidzacurukitsa mbeu za Davide mtumiki wanga, ndi Alevi akunditumikira Ine.
23. Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya, kuti,
24. Kodi sulingalira comwe anena anthu awa, kuti, Mabanja awiri amene Yehova anawasankha, wataya iwo? comweco anyoza anthu anga, kuti asakhalenso mtundu pamaso pao.