1. Amati, Ngati mwamuna acotsa mkazi wace, ndipo amcokera iye, nakhala mkazi wa wina, kodi adzabweranso kwa mkaziyo? dzikolo kodi silidzaipitsidwa? Koma iwe wacita dama ndi mabwenzi ambiri; koma bweranso kwa Ine, ati Yehova.
2. Kwezera maso ako ku mapiri oti se, nuone: sanagona ndi iwe kuti? Panjira wakhalira iwo, monga M-arabu m'cipululu; ndipo waipitsa dziko ndi zigololo zako, ndi zoipa zako.