Amati, Ngati mwamuna acotsa mkazi wace, ndipo amcokera iye, nakhala mkazi wa wina, kodi adzabweranso kwa mkaziyo? dzikolo kodi silidzaipitsidwa? Koma iwe wacita dama ndi mabwenzi ambiri; koma bweranso kwa Ine, ati Yehova.