Ndipo akumwela adzakhala nalo phiri la Esau colowa cao; ndi iwo a kucidikha adzakhala nalo dziko la Afilisti; ndipo adzakhala nayo minda ya Efraimu, ndi minda ya Samariya colowa cao; ndi Benjamini adzakhala nalo la Gileadi.