9. Wokondedwa wanga akunga mphoyo, pena mwana wa mbawala:Taona, aima patseri pa khoma pathu,Apenyera pazenera, Nasuzumira pamade.
10. Wokondedwa wanga analankhula, nati kwa ine,Tauka, bwenzi langa, wokongola wanga, tiye.
11. Pakuti, taona, cisanu catha,Mvula yapita yaleka;
12. Maluwa aoneka pansi;Nthawi yoyimba mbalame yafika,Mau a njiwa namveka m'dziko lathu;
13. Mkuyu uchetsa nkhuyu zace zosakhwima,Mipesa niphuka,Inunkhira bwino.Tauka, bwenzi langa, wokongola wangawe, tiyetu.
14. Nkhunda yangawe, yokhala m'ming'alu ya thanthwe, mobisika motsetsereka,Ndipenye nkhope yako, ndimve manako;Pakuti mau ako ngokoma, nkhope yako ndi kukongola.