28. Ndipo wansembe acite comtetezera munthu wakulakwa, osalakwa dala pamaso pa Yehova, kumcita comtetezeraj ndipo adzakhululukidwa.
29. Kunena za wobadwa m'dziko mwa ana a Israyeli, ndi mlendo wakukhala pakati pao, mukhale naco cilamulo cimodzi kwa iye wakucita kanthu kosati dala.
30. Koma munthu wakucita kanthu dala, ngakhale wobadwa m'dziko kapena mlendo, yemweyo acitira Yehova mwano; ndipo munthuyo amsadze pakati pa anthu a mtundu wace.
31. Popeza ananyoza mau a Yehova, nathyola lamulo lace; munthuyu amsadze konse; mphulupulu yace ikhale pa iye.
32. Ndipo pokhala ana a Israyeli m'cipululu, anapeza munthu wakufuna nkhuni tsiku la Sabata.
33. Ndipo amene adampezawo alinkufuna nkhuni anabwera naye kwa Mose ndi Aroni, ndi kwa khamu lonse.