Pompo ndinatama kusekaseka, pakuti munthu alibe kanthu kabwino pansi pano, koma kudya ndi kumwa, ndi kusekera; ndi kuti zimenezi zikhalebe naye m'bvuto lace masiku onse a moyo wace umene Mulungu wampatsa pansi pano.