12. Ndidzakumemezani ndithu, Yakobo, inu nonse; ndidzasonkhanitsa ndithu otsala a Israyeli; ndidzawaika pamodzi ngati nkhosa za ku Boma; ngati zoweta pakati pa busa pao adzacita phokoso cifukwa ca kucuruka anthu.
13. Wotyola wakwera pamaso pao; iwo anatyola, napita kucipata, naturuka pomwepo; ndi mfumu yao yapita pamaso pao, ndipo Yehova awatsogolera.