11. Adziwa mphamvu ya mkwiyo wanu ndani,Ndi ukali wanu monga ayenera kukuopani?
12. Mutidziwitse kuwerenga masiku athu motero,Kuti tikhale nao mtima wanzeru.
13. Bwerani, Yehova; kufikira liti?Ndipo alekeni atumiki anu.
14. Mutikhutitse naco cifundo canu m'mawa;Ndipo tidzapfuula mokondwera ndi kukondwera masiku athu onse.
15. Tikondweretseni monga mwa masiku mudatizunzawa,Ndi zaka tidaona coipa.
16. Cocita Inu cioneke kwa atumiki anu,Ndi ulemerero wanu pa ana ao.