5. Onani, ndinabadwa m'mphulupulu:Ndipo mai wanga anandilandira m'zoipa.
6. Onani, Inu mukondwera ndi zoonadi m'malo a m'katimo;Ndipo m'malo a m'tseri mudzandidziwitsa nzeru.
7. Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera;Munditsuke ndipo ndidzakhala wa mbu woposa matalala.
8. Mundimvetse cimwemwe ndi kusekera:Kuti mafupawo munawatyola akondwere.
9. Muzibisire nkhope yanu zolakwa zanga,Ndipo mufafanize mphulupulu zanga zonse.
10. Mundilengere mtima woyera, Mulungu;Mukonze mzimu wokhazikika m'kati mwanga.
11. Musanditaye kundicotsa pamaso panu;Musandicotsere Mzimu wanu Woyera.