1. Mundicitire ine cifundo, Mulungu,Monga mwa kukoma mtima kwanu;Monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanuMufafanize macimo anga.
2. Mubwereze kunditsuka mphulupulu yanga,Ndipo mundiyeretse kundicotsera coipa canga,
3. Cifukwa ndazindikira macimo anga;Ndipo coipa canga ciri pamaso panga cikhalire:
4. Pa Inu, Inu nokha, ndinacimwa,Ndipo ndinacicita coipaco pamaso panu:Kuti mukhale wolungama pakulankhula Inu,Mukhalenso woyera pa kuweruza kwanu.