1. Mulungu, tidamva m'makutu mwathu, makolo athu anatisimbira,Za nchitoyo mudaicita masiku ao, masiku akale.
2. Inu munapitikitsa amitundu ndi dzanja lanu, koma iwowa munawaoka;Munasautsa mitundu ya anthu, ndipo munawaingitsa,
3. Pakuti sanalanda dziko ndi lupanga lao,Ndipo mkono wao sunawapulumutsa:Koma dzanja lanu lamanja, ndi mkono wanu, ndi kuunika kwa nkhope yanu.Popeza munakondwera nao,
4. Inu ndinu mfumu yanga, Mulungu:Lamulirani cipulumutso ca Yakobo.