4. Pakuti asanafike mau pa lilime langa,Taonani, Yehova, muwadziwa onse.
5. Munandizinga kumbuyo ndi kumaso,Nimunaika dzanja lanu pa ine.
6. Kudziwa ici kundilaka ndi kundidabwiza:Kundikhalira patali, sindifikirako.
7. Ndidzapita kuti kuzembera mzimu wanu?Kapena ndidzathawira kuti kuzembera nkhope yanu?
8. Ndikakwera kumka kumwamba, muli komweko;Kapena ndikadziyalira ku Gehena, taonani, muli komweko.
9. Ndikadzitengera mapiko a mbanda kuca,Ndi kukhala ku malekezero a nyanja;
10. Kungakhale komweko dzanja lanu lidzanditsogolera,Nilidzandigwira dzanja lanu lamanja.
11. Ndipo ndikati, Koma mdima undiphimbe,Ndi kuunika kondizinga kukhale usiku:
12. Ungakhale mdima sudetsa pamaso panu,Koma usiku uwala ngati usana:Mdima ukunga kuunika.
13. Pakuti Inu munalenga imso zanga;Munandiumba ndisanabadwe ine.
14. Ndikuyamikani cifukwa kuti cipangidwe canga ncoopsa ndi codabwiza;Nchito zanu nzodabwiza;Moyo wanga ucidziwa ici bwino ndithu.
15. Thupi langa silinabisikira Inu popangidwa ine mobisika,Poombedwa ine monga m'munsi mwace mwa dziko lapansi.