13. Monga atate acitira ana ace cifundo,Yehova acitira cifundo iwo akumuopa Iye.
14. Popeza adziwa mapangidwe athu;Akumbukila kuti ife ndife pfumbi.
15. Koma munthu, masiku ace akunga udzu;Aphuka monga duwa la kuthengo.
16. Pakuti mphepo ikapitapo pakhala palibe:Ndi malo ace salidziwanso.
17. Koma cifundo ca Yehova ndico coyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye,Ndi cilungamo cace kufikira kwa ana a ana;
18. Kwa iwo akusunga cipangano cace,Ndi kwa iwo akukumbukila malangizo ace kuwacita.
19. Yehova anakhazika mpando wacifumu wace Kumwamba;Ndi ufumu wace ucita mphamvu ponsepo,
20. Lemekezani Yehova, inu angelo ace;A mphamvu zolimba, akucita mau ace,Akumvera liu la mau ace.
21. Lemekezani Yehova, inu makamu ace onse;Inu atumiki ace akucita comkondweretsa Iye,
22. Lemekezani Yehova, inu, nchito zace zonse,Ponse ponse pali ufumu wace:Lemekeza Yehova, moyo wanga iwe.