7. ndi ng'ombe zako, ndi nyama ziri m'dziko lako; zipatso zace zonse zikhale cakudya cao.
8. Ndipo uziwerengera masabata a zaka asanu ndi awiri, zaka zisanu ndi ziwiri kasanu ndi kawiri; kotero kuti zaka za masabata a zaka asanu ndi awiri, zifikire zaka makumi anai kudza zisanu ndi zinai.
9. Pamenepo uzitumizira lipenga lomveka m'mwezi wacisanu ndi ciwiri, tsiku lakhumi la mweziwo; tsiku la citetezero mutumizire lipenga lifikire m'dziko lanu lonse.
10. Ndipo mucipatule caka ca makumi asanu, ndi kulalikira kwa onse okhala m'dzikomo kuti akhale aufulu; muciyese caka coliza lipenga; ndipo mubwerere munthu ali yense ku zace zace, ndipo mubwerere yense ku banja lace.
11. Muciyese caka ca makomi asanuco coliza lipenga, musamabzala, kapena kuceka zophuka zokha m'mwemo; kapenakuceka mphesa zace za mipesa yosadzombola.
12. Popeza ndico caka coliza lipenga; muciyese copatulika, mudye zipatso zace kunja kwa munda.
13. Caka coliza lipenga ici mubwerere nonse ku zace zace.