10. Mapiri anakuonani, namva zawawa;Cigumula ca madzi cinapita;Madzi akuya anamveketsa mau ace,Nakweza manja ace m'mwamba.
11. Dzuwa ndi mwezi zinaima njera mokhala mwao;Pa kuunika kwa mibvi yanu popita iyo.Pa kung'anipa kwa nthungo yanu yonyezimira.
12. Munaponda dziko ndi kulunda,Munapuntha amitundu ndi mkwiyo.
13. Munaturukira cipulumutso ca anthu anu,Cipulumutso ca odzozedwa anu;Munakantha mutu wa nyumba yawoipa,Ndi kufukula maziko kufikira m'khosi.
14. Munapyoza ndi maluti ace mutu wa ankhondo ace;Anadza ngati kabvumvulu kundimwaza;Kukondwerera kwao kunanga kufuna kutha ozunzika mabisika.
15. Munaponda panyanja ndi akavaloanu,Madzi amphamvu anaunjikana mulu.