12. Ndipo panali ndi ife mnyamata, Mhebri, kapolo wa kazembe wa alonda, ndipo ife tinafotokozera iye, ndipo iye anatimasulira ife maloto athu; kwa munthu yense monga mwa loto lace anatimasulira.
13. Ndipo panali monga momwe iye anatimasulira, momwemo mudacitika; ine anandibwezera mu utumiki wanga, mnzanga anampacika.
14. Ndipo Farao anatumiza nakaitana Yosefe; ndipo anamturutsa iye msanga m'dzenjemo: ndipo iye anameta, napindula malaya ace, nalowa kwa Farao.
15. Farao ndipo anati kwa Yosefe, Ine ndalota loto, koma palibe wondimasulira; ndipo ndamva alikunena za iwe kuti, ukamva loto udziwa kumasulira.
16. Ndipo Yosefe anayankha Farao kuti, Si mwa ine; koma Mulungu adzayankha Farao mwamtendere.
17. Ndipo Farao ananena kwa Yosefe, M'loto langa taona, ndinaima m'mphepete mwa nyanja;
18. ndipo taona, zinaturuka m'nyanjamo ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri, zonenepa ndi za maonekedwe abwino; ndipo zinadya m'mabango;