9. Ndipo wopereka cikho wamkuru anafotokozera Yosefe loto lace, nati kwa iye, M'kulota kwanga, taona, mpesa unali pamaso panga:
10. ndipo m'mpesamo munali nthambi zitatu: ndipo unali wonga unaphuka, ndipo maluwa ace anaphuka; nabala matsamvu ace mphesa zakuca:
11. ndipo cikho ca Farao cinali m'dzanjalanga: ndipo ndinatenga mphesa, ndi kufinyira m'cikho ca Farao ndi kupereka cikho m'dzanja la Farao.
12. Ndipo Yosefe anati kwa iye, Mmasuliro wace ndi uwu: nthambi zitatu ndizo masiku atatu;
13. akali masiku atatu Farao adzatukula mutu wako, nadzabwezera iwe nchito yako; ndipo udzapereka cikho ca Farao m'dzanja lace, monga kale lomwe m'mene unali wopereka cikho cace.
14. Koma undikumbukire ine m'mene kudzakhala bwino ndi iwe, ndipoundicitiretu ine kukoma mtima: nundichule ine kwa Farao, nunditurutse ine m'nyumbamu:
15. cifukwa kuti ndinabedwa ndithu m'dziko la Ahebri; ndiponso pano sindinacite kanthu kakundiikira ine m'dzeniemu.
16. Pamene wophika mkate anaona kuti mmasuliro wace unali wabwino, iye anati kwa Yosefe, Inenso ndinalimkulota, ndipo, taonani, malicero atatu a mikate yoyera anali pamtu panga;
17. m'licelo lapamwamba munali mikate ya Farao ya mitundu mitundu; ndipo mbalame zinadya ya m'licelo la pamutu panga.