15. Pamene kunaca, amithengawo anafulumiza Loti, nati, Uka, tenga mkazi wako, ndi ana ako akazi awiri amene ali kunowa, kuti munganyeke m'mphulupulu ya mudzi.
16. Koma anacedwa; ndipo anthuwo anamgwira dzanja lace, ndi dzanja la mkazi wace ndi dzanja la ana ace akazi awiri; cifukwa ca kumcitira cifundo Yehova; ndipo anamturutsa iye, namuika kunja kwa mudzi.
17. Ndipo panali pamene anawaturutsa iwo kunja, anati, Tapulumuka ndi moyo wako; usaceuke, usakhale pacigwa pali ponse; thawira kuphiri, kuti unganyeke.
18. Ndipo Loti anati kwa iwo, Iaitu, mfumu;
19. taonanitu, kapolo wanu anapeza ufulu pamaso panu, ndipo munakuza cifundo canu, cimene munandicitira ine, pakupulumutsa moyo wanga; ine sindikhoza kuthawira kuphiri kuti cingandipeze ine coipaco ndingafe:
20. taonanitu, mudzi uwu uli pafupi pothawirapo, ndipo uli wong'ono; ndithawiretu kumeneko, suli wong'ono nanga? ndipo ndidzakhala ndi moyo.
21. Ndipo anati kwa iye, Taona, ndikubvomereza iwe pamenepanso kuti sindidzaononga mudzi uwu umene wandiuza.
22. Fulumira, thawira kumeneko; pakuti sindithai kucita kanthu usadafike kumeneko. Cifukwa cace anacha dzina la mudziwo Zoari.