Ndipo ndidzamdalitsa iye, ndiponso ndidzakupatsa iwe mwana wamwamuna wobadwa mwa iye, inde, ndidzamdalitsa iye, ndipo adzakhala amace a mitundu, mafumu a anthu adzaturuka mwa iye.