34. Ndi zidundumwa zace zinaloza ku bwalo lakunja; ndi pa nsanamira zace panali akanjedza cakuno ndi cauko; ndipo pokwerera pace panali makwerero asanu ndi atatu.
35. Pamenepo anabwera nane ku cipata ca kumpoto, naciyesa monga mwa miyeso yomweyi;
36. zipinda zace, makhoma a pakati pace, ndi zidundumwa zace; ndimo munali mazenera m'menemo pozungulirapo, m'litali mwace mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwace mikono makumi awiri mphambu isanu.
37. Ndi nsanamira zace zinaloza ku bwalo lakunja; ndi pa nsanamira zace panali akanjedza cakuno ndi cauko; ndipo pokwerera pace panali makwerero asanu ndi atatu.
38. Ndipo pa nsanamira za pazipata panali kanyumba ndi citseko cace; pamenepo anatsuka nsembe vopsereza.
39. Ndipo m'khonde la pacipata munali magome awiri cakuno, ndi magome awiri cauko, kuti apherepo nsembe yopsereza, ndi nsembe yaucimo, ndi nsembe yoparamula.