Pakupemphera Ezara tsono, ndi kuulula ndi kulira misozi, ndi kudzigwetsa pansi pakhomo pa nyumba ya Mulungu, udamsonkhanira mwa Israyeli msonkhano waukuru ndithu wa amuna, ndi akazi, ndi ana; popeza anthu analira kulira, kwakukuru.